Revelation 15:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.