Revelation 15:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mudatuluka angelo asanu ndi aŵiri aja okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri, atavala nsalu zoyera zambee, nkumangira malamba agolide pa chifuwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anatuluka m'Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼnyumbamo munatuluka angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri. Angelowo anavala nsalu zoyera bwino zonyezimira ndi malamba agolide pa zifuwa zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka m'Kacisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala mwala woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolidi pacifuwa pao,