Revelation 15:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chidapereka mikhate isanu ndi iŵiri yagolide kwa angelo asanu ndi aŵiri aja. Mikhateyo inali yodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kenaka chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cimodzi ca zamoyo zinai cinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.