Revelation 15:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'malo Opatulika aja mudaadzaza utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake. Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuloŵa m'Malo Opatulikawo mpaka itatha miliri isanu ndi iŵiri ija imene anali nayo angelo asanu ndi aŵiri aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Nyumba ya Mulungu inadzaza ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake, ndipo panalibe yemwe akanalowa mʼNyumbayo mpaka miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja itatha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Kacisi anadzazidwa ndi utsi wocokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yace; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kacisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.