Revelation 16:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamva mau akuru ocokera kuKacisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.