Revelation 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wacisanu anatsanulira mbale yace pa mpando wacifumu wa cirombo; ndipo ufumu wace unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwace,