Revelation 16:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka ndidaona mizimu yonyansa itatu, yonga achule, ikutuluka wina m'kamwa mwa chinjoka chija, wina m'kamwa mwa chilombo chija, wina m'kamwa mwa mneneri wonama uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona motuluka m'kamwa mwa chinjoka, ndi m'kamwa mwa chilombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona moturuka m'kamwa mwa cinjoka, ndi m'kamwa mwa cirombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati acule;