Revelation 16:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imeneyi ndi ija timati mizimu yoipa imene imachita zozizwitsa. Imapita ponseponse kwa mafumu a pa dziko lapansi kukaŵaitana kuti adzabwere ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu lija la Mulungu Mphambe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti ali mizimu ya ziwanda zakucita zizindikilo; zimene zituruka kumka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikuru la Mulungu, Wamphamvuyonse.