Revelation 16:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake mu mlengalenga. Pomwepo kudamveka mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu wa m'Nyumba ya Mulungu. Adati, “Kwatha!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mumlengalenga; ndipo m'Kachisimo mudatuluka mau akulu, ochokera kumpando wachifumu ndi kunena, Chachitika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wacisanu ndi ciwiri anatsanulira mbale yace mumlengalenga; ndipo m'Kacisimo mudaturuka mau akuru, ocokera ku mpando wacifumu ndi kunena, Cacitika;