Revelation 16:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali 1 cibvomezi cacikuru cotero sicinaoneke ciyambire anthu padziko, cibvomezi colimba cotero, cacikuru cotero.