Revelation 16:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chimudzi chachikulucho chidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo wamkali wa mkwiyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 2 cimudzi cacikuruco cidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo 3 Babulo waukuru unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse cikho ca vinyo wamkali wa mkwiyo wace.