Revelation 16:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacoka woyamba, natsanulira mbale yace kudziko; ndipo kunakhala cironda coipa ndi cosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la cirombo nalambira fano lace.