Revelation 16:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Matalala akuluakulu adagwa pa anthu kuchokera kumwamba. Lililonse kulemera kwake pafupi makilogaramu 45. Ndipo anthu adanyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali woopsadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatsika kumwamba matalala akulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 5 anatsika kumwamba matalala akuru, lonse lolemera ngati talenti, nagwa pa anthu; ndipo anthu 6 anacitira Mulungu mwano cifukwa ca mliri wa matalala, pakuti m1iri wace nm waukuru ndithu.