Revelation 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mngelo wachiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake pa nyanja. Pomwepo madzi ake adasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Ndipo zamoyo zonse za m'nyanjamo zidafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wachiwiri anatsanulira mbale yake m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo waciwiri anatsanulira mbale yace m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.