Revelation 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amchitire ulemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukuru; ndipo anacitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amcitire ulemu.