Revelation 17:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi cirombo.