Revelation 17:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo adzacita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, cifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.