Revelation 17:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nyanga khumi unaona zija, pamodzi ndi chilombo chija, zidzadana naye mkazi wadamayo. Zidzamlanda zake zonse ndi kumsiya maliseche. Zidzadyako mnofu wake, kenaka nkumuponya pa moto kuti apserere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi cirombo, izi zidzadana ndi mkazi wacigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yace, nizidzampsereza ndi moto.