Revelation 17:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkaziyo adaavala zovala zofiirira ndi zamlangali, ndipo adaadzikongoletsa ndi golide, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. M'manja mwake anali ndi chikho chagolide chodzaza ndi zonyansa, ndi zoipa za ntchito zake zadama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golide, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m'dzanja lake chikho chagolide chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi anabvala cibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wace, ndi ngale; nakhala naco m'dzanja lace cikho cagolidi codzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za cigololo cace,