Revelation 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a anthu a Mulungu, ndi a anthu ophedwera umboni wa Yesu. Nditamuwona mkaziyo, ndidadabwa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu. Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukuru.