Revelation 17:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mngelo uja adandifunsa kuti, “Ukudabwiranji? Ndikuululira chinsinsi chake cha mkazi ameneyu, ndi cha chilombo chimene iye wakwerapo, chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa chifukwa ninji? Ine ndidzakuuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chilombo chakumbereka iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa cifukwa ninji? ine ndidzakuuza iwe cinsinsi ca mkazi, ndi ca cirombo cakumbereka iye, cokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.