Revelation 17:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilombo chimene unachiwona chija, kale chidaali chamoyo, koma tsopano sichilinso chamoyo. Chiyenera kutuluka kuchokera m'chiphompho chija kupita kukaonongedwa. Anthu onse okhala pa dziko lapansi, amene chilengedwere dziko lapansi maina ao sadalembedwe m'buku la amoyo, azidzadabwa poona chilombocho. Azidzadabwa poona kuti kale chidaali chamoyo koma tsopano sichilinso chamoyo, komabe m'tsogolo muno chidzaonekanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cirombo cimene unaciona cinaliko, koma kulibe; ndipo cidzaturuka m'phompho, ndi kunka kucitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo ciyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona cirombo, kuti cinaliko, ndipo kulibe, ndipo cidzakhalako.