Revelation 18:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibenso wogula malonda ao a golide, siliva, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu; nsalu zoyera, zofiirira, zasilika ndi zamlangali; mitengo yamitundumitundu yonunkhira; zinthu zamitundumitundu zopangidwa ndi mnyanga wanjovu, ndiponso ndi mitengo yamtengowapatali; zinthu zopangidwa ndi mkuŵa, chitsulo ndi mwala wokongola;
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
malonda a golide, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
malonda a golidi, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wace, ndi a ngale, ndi a nsaru yabafuta, ndi a cibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya pfungo lokoma, ndi cotengera ciri conse ca minyanga ya njobvu, ndi cotengera ciri conse camtengo wa mtengo wace wapatali, ndi camkuwa ndi cacitsulo, ndi cansangalabwi;