Revelation 18:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu. Unkavala nsalu zoyera, zofiirira ndi zamlangali. Unkadzikongoletsa ndi golide, ndiponso ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golide ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo adzalira mokuwa kuti, “ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu, iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira, ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuru wobvala bafuta ndi cibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wace, ndi ngale!