Revelation 18:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adadzithira fumbi kumutu, akulira ndi kumva chisoni kwambiri. Ankafuula kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu, mzinda umene anthu onse okhala ndi zombo zapanyanja adalemera nacho chuma chake. Koma pa ora limodzi lokha wasanduka bwinja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti, “Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe, kumene onse anali ndi sitima pa nyanja analemera kudzera mʼchuma chake! Mu ora limodzi wawonongedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anathira pfumbi pamitu pao, napfuula, ndi kulira, ndi kucita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, cifukwa ca kulemera kwace, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja.