Revelation 18:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adafuula mokweza mau ndi kunena kuti, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja! Wasanduka malo okhalamo mizimu yoipa, malo othaŵiramo mizimu yonse yonyansa, malo othaŵiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti: “ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’ Wasandulika mokhalamo ziwanda ndi kofikako mizimu yonse yoyipa ndi mbalame zonse zonyansa ndi zodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.