Revelation 18:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la oimba zeze, kapena la akatswiri a zoimbaimba, kapena la oliza chitoliro kapena lipenga. Mwa iwe simudzapezekanso konse mmisiri wa ntchito iliyonse. Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la kupera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mau a anthu oimba zeze, ndi a oimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo mmisiri aliyense wa machitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba, oyimba zitoliro, ndi lipenga. Mwa iwe simudzapezekanso mʼmisiri wina aliyense. Mwa iwe simudzapezekanso phokoso la mphero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mau a anthu oyimba zeze, ndi a oyimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo nunisiri ali yense wa macitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;