Revelation 18:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti adamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zadama. Mafumu a pa dziko lonse lapansi adachita naye chigololo, ndipo anthu amalonda a pa dziko lonse lapansi ankalemererapo pa zolakalaka zake zodziwunjikira chuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mayiko onse amwa vinyo ozunguza mutu wazigololo zake. Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo, ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anacita naye cigololo; ndipo ocita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyererakwace.