Revelation 18:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe iye ankanyadira chuma ndi zosangalatsa, momwemonso mumsautse ndi kumliritsa. Iyeyo mumtima mwake amati, ‘Ine pano, mfumu! Sindine mkazi wamasiye, sindidzaona konse zondiliritsa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri monga mwaulemerero ndi zolakalaka zimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati, ‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi, ine sindine wamasiye ndipo sindidzalira maliro.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga momwe unadzicitira ulemu, nudyerera, momwemo muucitire eouzunza ndi couliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwace, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.