Revelation 19:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati, “Aleluya! Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu ndi zake za Mulungu wathu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha izi ndinamva ngati mau akulu a khamu lalikulu m'Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti, “Haleluya! Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi ndinamva ngati a mau akuru khamu lalikuru m'Mwamba, liri kunena, Aleluya; cipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;