Revelation 19:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo maso ace ali lawi la moto, ndi pamutu pace pali nduwira zacifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma iye yekha.