Revelation 19:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwerani, mudzadye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi wa okwerapo, mnofu wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, ang'onoang'ono ndi akuluakulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang'ono ndi akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti 3 mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang'ono ndi akuru.