Revelation 19:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti maweruzo ace ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wacigololo wamkuru, amene anaipsa dziko ndi cigololo cace, ndipo anabwezera cilango mwazi wa akapolo ace pa dzanja lace la mkaziyo.