Revelation 19:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 5 cinagwidwa ciromboco, ndi pamodzi naco mneneri wonyenga amene adacita zizindikilo pamaso pace, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la cirombo, ndi iwo akulambira fano lace; 6 iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulfure: