Revelation 19:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu 24 aja, pamodzi ndi Zamoyo zinai zija, adadzigwetsa pansi moŵerama, napembedza Mulungu amene amakhala pa mpando wachifumu. Adayankha kuti, “Amen, Aleluya!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, nizinena, Amen; Aleluya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti, “Ameni, Haleluya!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wacifumu, nizinena, Amen; Aleluya.