Revelation 19:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikondwere ndi kusangalala, ndi kumtamanda, pakuti nthaŵi ya ukwati wa Mwanawankhosa uja yafika, mkwati wake wamkazi waukonzekera ukwatiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tiyeni tisangalale ndi kukondwera ndi kumutamanda! Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika, ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.