Revelation 2:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Efeso umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa uja wanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m'dzanja lake lamanja, ndi kuyenda pakati pa ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba; Izi azinena iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lace lamanja, iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi: