Revelation 2:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena ainu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala naco cisautso masiku khumi. Khala wokholupirfka kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.