Revelation 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuti: Ndikudziŵako kumene inuyo mumakhala, ndiye kuti kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Inu ndinu okhulupirika kwa Ine, simudataye chikhulupiriro chanu, ngakhale pa nthaŵi ya Antipa, mboni yanga, munthu wanga wokhulupirika. Paja iye uja adamuphera kwanu komwe, kumene amakhala Satana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wacifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza cikhulupiriro canga, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.