Revelation 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu ndiri nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira ciphunzitso ca Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye cokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nacite cigololo.