Revelation 2:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Tiatira umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Mwana wa Mulungu, uja ali ndi maso onyezimira ngati malaŵi a moto, ndi mapazi onga chitsulo choŵala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lembera mngelo wampingo wa ku Tiyatira kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa Mwana wa Mulungu, amene maso ake ali ngati moto woyaka ndi mapazi ake ngati chitsulo chonyezimira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiyatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ace ngati lawi la moto, ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira: