Revelation 2:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu ndiri nako kotsutsana ndi iwe, cuti ulola mkazi 2 Yezebeli, wodzieha zekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasokeretsa akapolo anga, kuti acite cigololo ndi kudya zoperekedwa nsenbe kwa mafano.