Revelation 2:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana akenso ndidzaŵapha. Motero mipingo yonse idzazindikira kuti Ine ndine uja ndimadziŵa za m'mitima mwa anthu ndi za m'maganizo mwao. Aliyense mwa inu ndidzachita naye molingana ndi ntchito zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaononga ana ace ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti 3 ine ndine iye amene ayesa imso ndi mitima; ndipo 4 ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa nchito zanu.