Revelation 2:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma enanu a ku Tiatira simudatsate nao chiphunzitso choipachi, ndipo simudaphunzireko zimene iwo amati zinsinsi zozama za Satana. Kwa inu mau anga ndi akuti sindikuwonjezerani malamulo ena,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ndikunena kwa enanu a ku Tiyatira, kwa inu amene simunatsate chiphunzitso cha mkaziyo ndipo simunaphunzire zimene iwo amati ndi ‘zinsinsi zonama’ za Satana. Kwa inu mawu anga ndi akuti sindikuwunjikirani malamulo ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiyatira, onse amene alibe ciphunzitso ici, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.