Revelation 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani tsono kuti munali okwera kwambiri musanagwe; nchifukwa chake mutembenuke mtima, muzichitanso zija munkachita poyambazi. Mukapanda kutero, ndidzabwera nkudzachotsa ndodo ya nyale yanu pamalo pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani kuti munagwa kuchokera patali. Lapa ndikuchita zinthu zimene unkachita poyamba. Ngati sulapa ndidzabwera ndikukuchotsera choyikapo nyale chako pamalo pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero kumbukila kumene wagwerako, nulape, nucite nchito zoyamba; koma ngari sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa coikapo nyali cako, kucicotsa pamalo pace, ngati sulapa.