Revelation 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuti: Ndikudziŵa masautso anu ndiponso umphaŵi wanu, koma kwenikweni ndinu olemera. Ndikudziŵanso zomwe amakusinjirirani anthu amene amanama kuti ndi Ayuda, pamene sali Ayuda konse, koma ndi a mpingo wa Satana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.