Revelation 20:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya mota ndi sulfure, kumeneko kulinso ciromboco ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.