Revelation 20:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adachiponya m'Chiphompho muja, nachitsekera nkumatirira potsekerapo kuti chisadzanyengenso mitundu ya anthu mpaka zitatha zaka zija chikwi chimodzi. Zitatha zakazo ayenera kudzachimasulanso nthaŵi pang'ono.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikilo pamwamba pace, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka cikwi; patsogolo pace ayenera kumasulidwa iye kanthawi.