Revelation 20:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona mipando yachifumu, ndipo okhala pamipandopo adapatsidwa mphamvu zoweruzira milandu. Ndidaonanso mizimu ya anthu amene adaŵadula pakhosi chifukwa cha kuchitira Yesu umboni, ndiponso chifukwa cha kulalika mau a Mulungu. Iwowo sadapembedze nao chilombo chija kapena fano lake lija, ndipo adakana kulembedwa chizindikiro chija pa mphumi kapena pa dzanja. Adakhalanso ndi moyo nkumalamulira pamodzi ndi Khristu zaka chikwi chimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chilombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaona mipando yacifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa ciweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi cifukwa ca umboni wa Yesu, ndi cifukwa ca mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira cirombo, kapena fano lace, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nacita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka cikwi.