Revelation 20:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo iyeyo adzapita nanyenga Gogi ndi Magogi. Imeneyi ndi mitundu ya anthu okhala ku mphepo zonse zinai. Satana adzaŵasonkhanitsa pamodzi kuti achite nkhondo. Kuchuluka kwao ndi ngati mchenga wakunyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mungodya zinai za dziko, Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nadzaturuka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa acite nkhondo: ciwerengero cao ca iwo amene cikhala ngati mcenga wa kunyanja.